Munasiya
Munasiya
AfroReggie
 1 Munasiyatu
 Dziko lanulo,
 E, chifukwa cha ine;
 Ndi ku Betlehemuko
 Pakubadwa Inu,
 Nyumba zawo 'nakukanani.

 Mbuye Yesu, lowani m'mtima,
 Nyumba yanu ndi mtimanga.
 Mbuye Yesu lowani m'mtima,
 Nyumba yanu ndi mtimanga.

 2 Akumwambawo
 Naimbitsatu
 Kukulemekezani;
 Koma monga mwana
 M'dziko munabadwa,
 Munadzichepetsadi.

 3 Nyama za m'thengo
 Ndi mbalamezo
 Zili nazo zogonamo,
 Koma Mwana wa Mlungu
 Analibe nyumba,
 M'mapululu nagonatu.

 4 Munadzera ndi
 Mawu a moyo
 Akupulumutsa anthu;
 Anakaniza,
 Anasautsa,
 Anapachika Inu.

 5 M'mene mubwera
 Kutiweruza
 Ndi angelo aimbira,
 Mundiitane,
 Muti , "Idza 'we,
 Khala nane Kumwamba."

 Mtima wanga udzakondwera,
 M'mene mundilandiranso.
 Mtima wanga udzakondwera,
 M'mene mundilandiranso.