
Munasiya
AfroReggie
1 Munasiyatu Dziko lanulo, E, chifukwa cha ine; Ndi ku Betlehemuko Pakubadwa Inu, Nyumba zawo 'nakukanani. Mbuye Yesu, lowani m'mtima, Nyumba yanu ndi mtimanga. Mbuye Yesu lowani m'mtima, Nyumba yanu ndi mtimanga. 2 Akumwambawo Naimbitsatu Kukulemekezani; Koma monga mwana M'dziko munabadwa, Munadzichepetsadi. 3 Nyama za m'thengo Ndi mbalamezo Zili nazo zogonamo, Koma Mwana wa Mlungu Analibe nyumba, M'mapululu nagonatu. 4 Munadzera ndi Mawu a moyo Akupulumutsa anthu; Anakaniza, Anasautsa, Anapachika Inu. 5 M'mene mubwera Kutiweruza Ndi angelo aimbira, Mundiitane, Muti , "Idza 'we, Khala nane Kumwamba." Mtima wanga udzakondwera, M'mene mundilandiranso. Mtima wanga udzakondwera, M'mene mundilandiranso.